Chawa Farms

Chawa Farms Chawa Farms is an agro dealer and a farm with speciality in Maize farming

13/08/2026

Mitengo ya chimanga yayamba kukwera m'madera osiyanasiyana m'dziko muno kuphatikizapo m'maboma aku chigwa cha mtsinje wa Shire komwe m'misika ina chimangachi chafika K60,000 pa thumba lolemera makilogalamu 50.

Ku Nsanje, chimanga amachigulitsa pa mitengo ya pakati pa K50,000 ndi K55,000 mwezi wathawu, ndipo pano chafika pa K60,000, thumba lolemera makilogalamu 50.

Ku Chikwawa, chimanga m'misika ina amachigulitsa pa mitengo ya pakati pa K45,000 ndi K50,000 mwezi wathawu, koma pano ena akuchigulitsa pa mitengo ya pakati pakati pa K55,000 komanso K60,000 thumba lolemera ma kilogalamu 50.

Mkulu oona za ulimi m'boma la Chikwawa, a Isaac Alli, wati kukwera kwa chimangachi ndi kaamba koti anthu ku chigwa cha m'tsinje wa Shire akudalira chimanga chochokera m'madera ena ponena kuti sanakolole chifukwa cha ng'amba ndi madzi osefukira zomwe zidawononga mbeu.

Padakali pano, m'boma la Ntcheu, mchigawo cha pakati, chimangachi chakwera kufika pa K40,000 thumba lolemera makilogalamu 50 kuchoka pa mitengo ya pakati pa K30,000 ndi K35,000 ndipo m'madera aku mpoto maka ku Mzimba, tsopano chili pa K47,000 kuchoka pa K36,000 thumba lolemera makilogalamu 50.

Source: ZBSNews

This is how we start the winter cropping, red onions....watch the space as we provide more updates..
17/07/2026

This is how we start the winter cropping, red onions....watch the space as we provide more updates..

Address

Lilongwe
265

Website

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when Chawa Farms posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Shortcuts

Share

Category