22/09/2026
๐ฑTIKUTEROTU NKHANI ZAKE KUTI MUKAKOLOLA SIKUTI NTCHITO YATHERA PAMENEPO AYI!
Folo TreeWorld Nurseries
Foni: 0881883469
Alimi ambiri akakolola, amasiya zotsalira m'munda monga:
๐ Masamba ndi tsinde la nthochi
๐ Nthochi zowola kapena zomwe zagwa pansi
๐
Tomato owola ndi zipatso zomwe zagwa
Zotsalirazi zingakhale malo obisalamo ndi kusungiramo tizilombo toyambitsa matenda.
Zitha kuthandiza kuti mavuto monga:
๐ฆ Chiwawu komaso kafota
๐ Kodi muyenera kuchita chiyani mukakolola?
๐ Yang'anani m'munda.
โ๏ธ Sosani kapena chotsani zotsalira kuzokolora zanu
๐งน Chotsani zipatso zowola ndi zomwe zagwa pansi.
๐ซ onetsetsani musasiye zotsalira za mbewu zodwala kwa nthawi yayitali zikadali munda musadasose or kuchotsa.
๐ฑ Pewani kusamutsira zotsalira zodwala ku munda wina.
๐ Nthochi imene mwakolora onetsatsani kuti mwachotsa zotsalira monga masamba komaso thunthu lake lija ndi kulikwira or kuwotcha ena amadyetsa ziweto. Koma osangozisiya mmunda wanu ayi zitha kupereka mwayi wakuti matenda achulukane
๐ก Nโchifukwa chiyani izi ndi zofunika?
Kusamalira zotsalira za mbewu kungathandize kuchepetsa:
โ Matenda m'munda
โ Kuchuluka kwa tizilombo
โ Kuwonongeka kwa mbewu
โ Zipatso zosakhala bwino
โ Matenda kubwereranso mu mbewu yotsatira
๐ฑ๐๐
Munda waukhondo mukakolola ndi gawo la ulimi wabwino.
TreeWorld Nurseries
Kudzala mitengo, kuphunzitsa, kulimbikitsa ulimi wazipatso