Root-Rise Agribusiness

Root-Rise Agribusiness Practical farming solutions, input planning and agribusiness support for productive, market-oriented farming in Malawi.

NKHANI YABWINO KWA MLIMI OTSOGOLATakubweretserani ma Seedling Trays apamwamba pa mitengo yomvelera! Mwayiwu usakuphonyen...
08/05/2026

NKHANI YABWINO KWA MLIMI OTSOGOLA

Takubweretserani ma Seedling Trays apamwamba pa mitengo yomvelera! Mwayiwu usakuphonyeni:
200 Holes: K10,000
128 Holes: K8,000

Tikupezeka ku Mzuzu pa Junction ya Bishop ndi Mchengautuwa opposite Kazuni Filling Station koma timatumiza kulikonse! Tiyankhuleni pa +265897035345.

Kodi ma pipe anu amaphulika-phulika chifukwa cha pressure ya pampu? Bwerani ku Root-Rise Agribusiness muzagule ma canvas...
15/04/2026

Kodi ma pipe anu amaphulika-phulika chifukwa cha pressure ya pampu? Bwerani ku Root-Rise Agribusiness muzagule ma canvas outlet pipe amphamvu kwambiri a 8 Bar!

Gulani zolimba zopindulitsa ulimi wanu wa Nthilira:
2 Inch 50 meters: MK 250,000
3 Inch 50 meters: MK 350,000
Ma pipe awa ndi olimba kwambiri, amapirira kutentha kwa dzuwa ndipo saphulika ndi pressure yamphamvu ya pampu yanu. Imbani 0897035345 kapena tipezeni ku office yathu ku Mzuzu.

10/04/2026

NKHANI YABWINO KWA MLIMI OTSOGOLA

Root-Rise Agribusiness yakubweretserani ma Seedling Trays apamwamba pa mitengo yomvelera! Mwayiwu usakuphonyeni:

200 Holes: K10,000
128 Holes: K8,000

Zomwe mupindule pogwiritsa ntchito ma Seedling Trays amenewa:
1. Mbande Zamphamvu: Mbande zanu zikhala zamphamvu komanso zathanzi.
2. Kupulumutsa Ndalama: Museva ndalama zanu

Tikupezeka ku Mzuzu koma timatumiza kulikonse! Tiyankhuleni pa +265897035345.

LELO TIPHUZITSANE ULIMI WA NYEMBA!Kodi mumadziwa kuti ulimi wa nyemba ndi imodzi mwa njira zachangu zopangira ndalama m'...
04/04/2026

LELO TIPHUZITSANE ULIMI WA NYEMBA!
Kodi mumadziwa kuti ulimi wa nyemba ndi imodzi mwa njira zachangu zopangira ndalama m'chaka cha 2026?

MBEU ZOMWE ZIMAPINDULITSA:

1. Nua-45 (Sugar Beans): ๐Ÿ’Ž
Ubwino: Ili ndi Iron ndi Zinc wambiri komanso imachita msanga (masiku 70-80).
Mtengo: Ku SeedCo kuyambira April azipanga K15,000 pa kg.

2. Kholophethe (Red Kidney): ๐Ÿ”ด
Imapirira chilala ndipo m'ma hotelo ndi m'mafakitale amaifuna kwambiri.

3. Kambidzi: ๐Ÿ”
Imapirira kwambiri matenda a masamba.

ZOYENERA KUCHITA:
Mbeu: Gwiritsani ntchito 30kg - 40kg pa ekala imodzi.
Crop Rotation: Musadzale pomwe panali nyemba chaka chatha; dzalani pomwe panali chimanga kapena fodya.

MAWERENGERO (Ekala Imodzi):
Ndalama zogwiritsa ntchito: pafupifupi K750,000+ (kuphatikiza mbeu, feteleza, ndi ganyu).
Zokolola: Matumba 15 mpaka 20 (50kg).
Phindu: Mukagulitsa bwino, m***a kupanga mpaka K4 Million+! ๐Ÿ’ธ๐Ÿ’ธ

Kodi inu mwakonzeka kudzala nyemba chaka chino? Siyani maganizo anu mu comment kapena funsani funso!
Tsatirani tsamba lathu kuti muzipeza upangiri wa Ulimi

Happy Chilembwe day
15/01/2026

Happy Chilembwe day

Zimene mungadziwe za Mbeu ya Hybrid ya ChimangaMbeu ya hybrid amayipasa ma siku oti iche kapena kunkhwima ndiye imafunik...
06/01/2026

Zimene mungadziwe za Mbeu ya Hybrid ya Chimanga

Mbeu ya hybrid amayipasa ma siku oti iche kapena kunkhwima ndiye imafunika kuyipasa chisamaliro mwachangu potengera masiku ake.

Mwachisadzo mbeu ya kalulu imakhala yakhwima pakamatha masiku 80 ndiye kuti imeneyi pakamatha 40 days imakhala yapota ndiye ngati mwachedwesa kuthira fertilizer sagwira ntchito, chimodzimodzi Kanyani ndiwa 90 days ndiye kuti paka matha masiku 50 amakhala wapota.

Mbeu zina ndi ma 105,120 days zomwe dzimacha mochedwa, izi zilibe vuto kwambiri pankhani ya fertilizer koma chinsinsi cha chimanga tiwonesese kuti kuchokera day 1 mpaka day 30 fertilizer yense tikhale tathira kuti chikure mwa nthanzi komanso chitipase ana akulu akulu๐ŸŒฑ

Tsatirani tsamba lathu kuti mupeze maupangiri ena a ulimi

KUSIYANA KWA KUTHIRA FETELEZA MOSIYANASIYANA:๐Ÿ”น NPK oyamba, Urea omaliza (osamikisa):Njira iyi imathandiza chomera kuland...
19/12/2025

KUSIYANA KWA KUTHIRA FETELEZA MOSIYANASIYANA:

๐Ÿ”น NPK oyamba, Urea omaliza (osamikisa):
Njira iyi imathandiza chomera kulandira zakudya panthawi yoyenera. NPK amathandiza kukula koyambirira (mizu, tsinde, masamba), pomwe Urea amathandiza kukula pa nthawi yokhwima. Iyi ndi njira yabwino kwambiri.

๐Ÿ”น Kumikisa NPK ndi Urea pamodzi:
Njira iyi imalimbikitsa masamba kwambiri osati zokolola, komanso imatha kuwononga mbeu.

Ndibwino kuthira NPK koyamba kenako Urea pa nthawi yoyenera osati kumikisa pamodzi.

Root-Rise Agribusiness
Tsatirani tsamba lathu kuti mupeze maupangiri ena a ulimi.

19/12/2025

Pump yabwino kwabasi, Honda 7.5 Horse Power Petrol Pump!!
Water Source yi mukuyiona bwanji?

MMENE TINGATETEZERE TOMATO KU BLOSSOM END ROTNthawi zina tomato amakula bwino, koma akayamba kucha mumapeza kuti pansi p...
18/12/2025

MMENE TINGATETEZERE TOMATO KU BLOSSOM END ROT

Nthawi zina tomato amakula bwino, koma akayamba kucha mumapeza kuti pansi pa tomato pamakhala chigamba chakuda. Izi zimatchedwa Blossom End Rot.

Zimayambitsidwa ndi:
โ€ข Kusowa kwa Calcium mโ€™nthaka kapena mโ€™mbewu
โ€ข Nthaka yokhala ndi acid yambiri (pH yotsika) yomwe imalepheretsa kuyamwa Calcium
โ€ข Kusathilira madzi mokhazikika makamaka nthawi ya dzuwa lalikulu

Tingathetse bwanji?
โœ” Thirani lime kapena gypsum musanadzale kuti mukonze nthaka
โœ” Thilirani madzi nthawi zonse osasiya nthaka youma
โœ” Pa nthawi ya maluwa, gwiritsani Calcium Nitrate (CN) kapena Calcibor
โœ” Manyowa osakaniza ndi phulusa amathandizanso kuchepetsa acid
๐Ÿ‘‰ Sankhani njira imodzi kapena ziwiri malinga ndi nthaka yanu.

Root-Rise Agribusiness
Tsatirani tsamba lathu kuti mupeze maupangiri ena ofunikira pa ulimi.

In Malawi, research shows that many farming challenges are caused by weak planning, inefficient water use and poor linka...
17/12/2025

In Malawi, research shows that many farming challenges are caused by weak planning, inefficient water use and poor linkage between inputs and markets.
ROOT-RISE AGRIBUSINESS is a new agribusiness initiative focused on practical solutions that help farmers improve productivity and make better production decisions, starting with irrigation, farm management and input planning.

Over the coming months, we will be sharing field-based insights, practical tools and lessons from working with farmers and agripreneurs across the value chain.
Growth in agriculture starts from the roots.

Address

Mzuzu City
Mzuzu

Website

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when Root-Rise Agribusiness posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Share

Category