Simiyon super stories

Simiyon super stories Cholinga chathu ndikusangalatsa, kudziwitsa komaso kuphuzitsa

pangani follow page

WhatsApp

number 0893035000

16/04/2026

Big shout out to my newest top fans! AbdulRazaq Matola, Tasleem William, Happy Mateman, Alina Wa Njonjo, Agness Sandram, Angellah Chiwayu, Daniel Kapuza Bvumbwe, Doreen Mackphat, Dorothy Chaponda, Patrick Sandama, Privia Nahawa, Samfray MW, Lufeyo Chazama Bwatamira, Babrah Kavina, Davie Banda

15/04/2026

Big shout out to my newest top fans! AbdulRazaq Matola, Samfray MW, Tasleem William, Happy Mateman, Alina Wa Njonjo, Agness Sandram, Angellah Chiwayu, Daniel Kapuza Bvumbwe, Doreen Mackphat, Dorothy Chaponda, Patrick Sandama, Privia Nahawa, Lufeyo Chazama Bwatamira, Babrah Kavina, Davie Banda

15/04/2026

THE WRONG DECISION

Shot story

written by
Simiyoni Mwale

Osayiwala kupanga follow page yathu ya Simiyoni super stories kuti nkhani zina zisamakuphonyeni

TIYAMBE

"Amayi amene uja ndi M'nyamata wabwino kwambiri komanso ndi wolemela. Mukudziwa chani? Mwezi womweuno akuti andigulila iPhone moti tima phone ititi nditiponyela kutali kkk".Analankhula uku akuseka ntsikana.

Uyutu anali mwana wa a Jacob ndipo panthawiyi anali atangokhala pantengo wamasuku kucheza ndi amayi ake. Ili linari banja lovutika ndithu ndipo kuti apeze chakudya amachita kupanga maganyu tsiku ndi tsiku.

Kunali kovuta kuti ntsikanayu akhoza kupitiliza School malo mwake anangopanga chiganizo chosiya. Atasiya choncho basitu amangokhala pakhomo nkumathandizana ntchito ndi makolo ake kwinaku masiku akupita. Kukamba mosabisa anali ntsikana wokongola moti ngakhale anabadwila kubanja lovutika koma ayi ndithu amayesetsa kuzisamalila zimene zimapangitsa kuti anyamata ena azidyelera maso.

Dzina lantsikanayu anali Tapiwa.

Apatu anapitiliza kucheza ndi amayi ake aja ndipo Amayi ake anayankha avekele..
"Zowonadi mwanawe kukwatila ndi mamuna amene uja nyengo zathu zikhoza kusintha. Ukuyenela kumamukonda basi mpakana azakutenge. Ndatopa ndi uphawi ine kkk".Nawoso atamaliza kulankhula amayi aja anaseka zimene zinapangitsa kuti macheza afike pamponda thobwa pamalo paja.

A Jacob Anali akuchokela kokamalizitsa kaganyu kena kamene anakasiya tsikulina. Atafika pakhomo anapeza mayi ndi mwana Wake atadekha pasi pantengo wamasuku kuthibula macheza. Atayima kaye anava nkhani zimene zikukambidwa pamene paja ndipo anatchela makutu kuti avetsetse.

Zinawatutumutsa mpaka sanaugwile ntima koma kufika uku akulankhula evekeke...
"Zanyasi zanuzo pakhomo panga pano ayi!. Mamamuna mukumunenayo simamuna wabwino or mpang'ono pomwe. Ndipo iwe!".Analankhula uku akuloza Tamala...
Usayelekeze kukwatilana ndi mamuna amene uja. Chuma mukuchinenacho chilibe ntchito, Ino sinthawi womakwatilila poti mwawonako chuma ayi. Mukuyenela kumasankha mamuna amene angakuthandizeni moyo wanu wonse, mamuna wachikondi, mamuna Wamakhalidwe abwino, Komanso mamuna Wozilemekeza".Anayima kaye kulankhula a Jacob uku akusiya pansi khasu kenako anapitiliza avekele...

"Ndikumudziwa bwino nyamatayo ndipo ndi M'nyamata wankhaza komanso wopanda umunthu. Chuma mukunenacho anatchita kudutsila munjila zosakhala bwino kuti achipeze. Osayelekeza kupanga zimenezo pezani mamuna wina osati Jose mukumunenayo".Analankhula zambiri bambo aja ndipo atangomaliza anakalowa munyumba mene anakapeza maungu kenako ananyamula mbale yamaungu ija nkumakadya pabwalo kwinanu akuvela kanyimbo ka Giboh Pearson.

THE WRONG DECISION

Continue...

Linali tsiku lina limene Jose Amafuna akakumane ndi Tapiwa. Apatu anakozeka mwana wamamuna ndipo atamaliza kukozeka kuja anatenga ka galimoto kamene amayendela ndipo anakafika pamalo pamene amakumanilana. Atafika pamalo paja anayimitsa galimoto yake ndipo kuti azitsika mugalimoto muja anaphana maso ndi bambo ake a Tapiwa uku maso awo tachita kufiwila ngati atandalila kutchisa kampopi.

Anayamba kulankhula madala aja avekele..
"Hey! Mwana wanjoka iwe!. Ukhale kutali ndi mwana wanga apo ayi uwona zimene nditakupange. Ungovutika mwana wanga sabwela kuno ungotaya nthawi yako pamenepo".Atangova izi nyamata uja ananyasidwa ndipo nayeso anayamba kubweza mau avekele...

"Heey! M'dala iwe! usayelekeze dala kuyima panjila yanga apo ayi ndipanga zayiwe!. Chimene mukumuletsela mwana wanu ndichani? Sindilola kumusiya ndipanga njila mpaka ndimukwatile basi".Analankhula mokwiya nyamata uja uku akulowa mugalimoto. Ndipo chokha chongokwela anamuwona Tapiwa akubwela koteloko uku akuthamanga. Apatu madala aja nawoso anali wodabwa ndipo samayembekezela kuti mwanayu akhoza kutulukila pamalopa.

Sanachedwe madala koma kulivumbulutsa fuso avekele...
"Heey! Ukatelo ukupita kuti? Ndamuyitanitsa James mwana wa Aphiri akuntunda aja kuti azakuwone, iwe ulikuno ukuzafuna chani?.
"Madala. James mukumunenayo ine sindikumufuna. Uyu ndi mamuna amene ineyo ndidasankha osati zogwa nchiswe mukuzinenazo".Anayankha mwana wankazi m'maso muli gwaa kwinaku akukadawila galimoto ngati muja achitila nanzikambe akamakwela muntengo.

Apatu abambo ake aja anangopukusa mutu wopanda m'nyanga ndipo mau awo wotsiliza amene analankhula mpaka Tapiwa kuwava anali woti asamuwonenso akubwela pakhomo pawo ndipo amawu awa anali akuzungulila mutu mwantsikanayo ngati nguli ya ntengo wa Nsenda luzi.

Galimoto inalira ndipo inachoka pamalo paja kuwasiya a Jacob akupita kunyumba uku manja atapindila munchiuno.
Atafika kunyumba anapenza nyamata wotchedwa kuti James uja atakhala pakhonde kumudikila Tapiwa kuti akumane naye. Atafika bambo aja anangofikula kuyamba kulankhula kuwalankhura akazi awo aja avekele...

"Anaphiri? Ndani anamutsekulila Tapiwa kuti atuluke munyumba? Mesa ndinanena ine kuti asatuluke munyumba kubwela mulendo!".Analankhula koma uku akukalipa madala aja.
"Ndinawona kuti madzi palibe pakhomo pano ndiye ndinamutuma kuti akatungeko madzi ndiye mwati wathawa?".Anafusa ngati sakudziwa kanthu mayi aja komatu pasi pantima amadziwa ndithu kuti anachitila dala.

Apatu kukangana kunafikapo moti Moti pamapeto pake nyamata uja anangodziwa zomapita kwawo. Kukamba za Tapiwa Kukwatiwa kunali komweko ndipo sanabwelenso pakhomo paja.

Masiku anali akupita ndithu moti pakupita kwanthawi Tapiwa anayamba kuyimba ma phone kuyimbila amayi ake kuwazonda. Ndipo amayi ake amayesela kudandaula kuti njala yavuta koma palibe chimene chimachitika. Ngakhale mamuna wa Tapiwa anali wolemela koma Samalora kuti Tapiwa agwile ndalama moti chilichonse amapanga ndiyeyo .

Iziti zinayamba kumupatsa maganizo Tapiwa ndipo Mamuna wake akachokapo kupita kuntchito amayesetsa kuti ayang'ane ndalama munyumbamo kuti mwina atumizile makolo ake koma ayi ndithu munyumbamo samapeza or ndi 10 kwacha yomwe. Izitu zinayamba kumudabwitsa Mwana wankazi ndipo zinayamba kumupatsa maganizo.

Anali akukhala ngati banja ndipo pakupita kwanthawi mamuna wake uja anayamba kumuchitila nkhaza Tapiwa ndipo anayamba kukhala ngati wantchoto osati nkazi wapakhomo. Zinayamba kumuwawa moti anayamba kukumbuka mau amamuwuza Madala ake aja. Zinthu zinafika paja poti anayamba kuganiza zolisiya banja.

THE WRONG DECISION

Tiyamba kuponya nkhani posachedwapa chonde musatalikilane ndi page ino kuti zokomazi zisamakuphonyeni.

Iyi inali Shot story chabe

Iyi ndikhani imene tikufuna kuti tiyipange tijambule Filimu.

Choncho tayisiyila kaye pomwepa

Ngati mukufuna kuti mulembi wanu Simiyoni Mwale apitilize kulemba nkhani pamudzi pano tapangani Share Shot story imeneyi kuti anzanuso apange follow page yathu.

Nkhani zilipo zikungofunika inuyo mutengepo gawo kupanga support page ino kuti ibwelele pakale.

Share, like, Comment,

💥🔥

Pangani follow page ya Simiyoni super stories

14/04/2026

Mawa ndiponya Shot story pano mukhale wokozeka 💥🔥

07/04/2026

Pano magobo nde anatha Zitengela imu kuti post ino muyipatsa ma likes angati tiyambenso kulemba nkhani

Tipushe music promo ikupanga zimenezi, pic imene mukuwona kuti sikuwoneka bwino iwowa akupanga kuti ikhale mbambande 🔥
01/04/2026

Tipushe music promo

ikupanga zimenezi, pic imene mukuwona kuti sikuwoneka bwino iwowa akupanga kuti ikhale mbambande 🔥

31/03/2026

Tizitolele kaye tiyambileso kulemba nkhani 🤣

WAR CHILDRENS 💥Chi filimu chimene chikutuluka lamulungu lino🔥Kozekelani ma bundle guys eee movie iyiyi ikhala mbambande ...
13/02/2026

WAR CHILDRENS 💥

Chi filimu chimene chikutuluka lamulungu lino🔥

Kozekelani ma bundle guys eee movie iyiyi ikhala mbambande guys

mukafuna kudziwa zambiri alankhuleni eni movie imeneyi pa number iyi

0982550349

06/02/2026

Big shout out to my newest top fans! Jayne Lackson, Wanangwa Banda, Tamie Chilembwe, Meya Tembo, Carolyn Stafford, Grace Phiri, Memori Banda, Jimmy Mbatata, Dorothy Chaponda, Wanangwa Zgambo, Stanley Chandida, Nemzy Makuta, Fortune Mnthali, Patrick Sandama, Kalingalire Bright, Stewart Victor Newa, Sallomy Rabson, AbdulRazaq Matola, Zione Mwale, Alinafe Baibe, Mphatso kaipa, Ellacy Chavula, Luwiza Edison, Khãlîfã Ñóspèr Çèè, Linly Mathiya, Tasleem William, Eluby Mailosi, Brenda Kamanga, Achilandanda Rajabuh, Maggie WA Nkhande, ۦٰٰٰٰٰٰۦٰٰٰٰٰٰ ۦٰٰٰٰٰٰۦٰٰٰٰٰٰ ۦٰٰٰٰٰٰۦٰٰٰٰٰٰ ۦٰٰٰٰٰٰۦٰٰٰٰٰٰ, Squecy Kate, Penuel Nyozani, Henry, Queen Sheera Somanje, Princess Mwanza, Happy Mateman, Grenar Juwawo Kokha, Tinashe Fatness Kudzula Phiri, Aggie Aggie, Naheem Chris, Sumiyat Sadiyat, Mercy Kamkwalala, Alina Wa Njonjo, Alex E Mical, Yvonne Trust, Angellah Chiwayu, Maggie Tizola, Florence Khoza, Ireen Mphande

Address

Kasungu

Telephone

+265982550349

Website

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when Simiyon super stories posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Shortcuts

Share

Category