Kufuna Kutchuka and Other Stories

Kufuna Kutchuka and Other Stories Kuphunzitsana za Mawu a Mulungu masiku Otsiriza chipulumutso chili pafupi Chivumbulutso 22:12.....Pastor Johnson Stanley Banda.

26/01/2026

Big shout out to my newest top fans! Mickson Chikapa, Ommie Kachepa Omega, Anne Mbodi, Anne Anny, Nthunthuwaka Adika, Naomie Malikebu, Wongani Namaja, Tinersh Malunga, Chipiliro Labeka, Christina Maseko, Testmony Caroline Kachingwe, Cathy Hankey, Trizar Sukasuka, Madah Mambo, Din Daniel Halawa, Piliran Banda, Sattie Chiwanga, Ireen Emmanuel, Enert Kalumbi, Diana Sidiwelo, Leticia Sanah, Simeon Ellity, Sharp Man, Mary Farook, Brandinah Jere, Fy Wa Banda, Rose Joy Fungulani, Fd Daniel, Ęg Dukuse, Chancy Chilenje, Rejoice Banda, Young Scott Bosses, Olive Kandoje, Promise Kachepa, Sellah Mkomandolo

Wodala Ali oyera mtima chifukwa adzaona Mulungu..Mateyu 5:8
21/01/2026

Wodala Ali oyera mtima chifukwa adzaona Mulungu..Mateyu 5:8

Am back after Long time School days...Thank you all my loved fans🙏🙏♥♥
12/10/2025

Am back after Long time School days...Thank you all my loved fans🙏🙏♥♥

26/03/2025

Amene afuna pageyi andiuze ine ndinasiya. Zikomo

30/10/2024

Shout out to my newest followers! Excited to have you onboard! Evolisto Mw, Raphael Christian Sannie Gama, Abel Amin Sugar, Chancy Chilenje, Flora Soko, Trintas Mpondawaya, Merry Gondwe, Esawu Abiseni, Brandina Walusa

*TIDZAFERA LIMODZI IWE NDI INE.*__PART 03__Okondedwa awerengi nonse, mongokumbutsana; pajatu mu part 2 tinalekeza pomwe ...
23/10/2024

*TIDZAFERA LIMODZI IWE NDI INE.*

__PART 03__

Okondedwa awerengi nonse, mongokumbutsana; pajatu mu part 2 tinalekeza pomwe mayi mfumu amauza mnzake wa Annabel uja kuti akuyenera kumapita chifukwa Prince Dan afunika acheze ndi mkazi wake. Kenako atapita, nawonso mfumukazi aja adakalowa kuchipinda kwao kusiya Prince uja ndi Annabel akucheza. Koma Prince Dan uja adati;.......

Tipitirize.......

Koma ataona prince Dan uja anaona kuti zoondi Annabel adali wokongola kwambiri. Ndipo adati; Oooh ukuonekadi wokongola monga mayi anga adandiuzira. Zikomo kwambiri mfumu yanga. Adatero Annabel uja. Kenako Annabel adati kwa Dan; mfumu yanga tiyeni nanga tikakhale kuchipinda kwanu nkutheka kuti mukundifuna. Koma Dan adayankha nati; kukufuna chani? Iwe ndi ine sitingakhale limodzi mpaka tidzakwatirane. Ndipo nthawi yomweyo adachoka prince uja naturuka panja kumusiya iye mnyumba muja.

Apa Annabel adali wokhumudwa pang'ono chifukwa amafuna kuti prince Dan uja apakulemo nyemba mu mphika wake. Koma kuja Loney uja business yake ya Makala imayenda bwino kwambiri ngakhale kuti amavutika kuchita kwake. Ndipo chifukwa choti nayi mfumu adamkonda kwambiri Annabel pa zifukwa zodziwa wokha, adapanga changu kuti ukwati uchitike. Kenako adalengezetsa tsiku lomwe utachitikire ukwati wa mwana wao.

Anthu onse adali wokonzeka ndithu kuti pasikuli akasangalala kwambiri. Tsiku la ukwati lija litakwana, anthu ambiri adasokhana kudikira kuonera ukwatiwu. Kona naye Loney atamva kuti X wake akupangitsa ukwati lero, adakana kuti iyeyo sapitako kukamuona mmalo mwake adatuma sister wake Tereza kuti apite limodzi ndi mamwana kake kaja. Ndipo kanali kasanasambeso ayi kamwana kaja kanangoti zimakala bii ku nkhope.

Atafika ku palace kuja, adapeza mwambo wa ukwati wayambika anthu akuvina kwinaku akuponya ndalama pansi. Tereza ndi Kamwana kaja adaima ku gate nayamba kuvina one zomwe zimaimba ku ukwatiko. Koma kamwana kaja kataona ndalama zomwe anthu amagwetsa zija, kanathamanga kuyamba k

*TIDZAFERA LIMODZI IWE NDI INE* __PART 02__Okondedwa awerengi nonse, mongokumbutsana mu part 1 tinalekeza pomwe mayi mfu...
19/10/2024

*TIDZAFERA LIMODZI IWE NDI INE*

__PART 02__

Okondedwa awerengi nonse, mongokumbutsana mu part 1 tinalekeza pomwe mayi mfumu aja adasintha kalata wachikondi kukhala wachidani ndipo adatuma mlonda kuti akapasire Loney uja. Ndipo atalandira kalata uja Loney adali ndi chimwemwe poganizira chikondi chao. Koma atatsegula kuyamba kuwerenga adati;........

Tipitirizee......

Ndipo mlonda uja adachoka napita ku palace. Ndipo Loney adayamba kuwerenga kalata uja. Akuwerenga kalata chonchija adati; zitheka bwanji kuti Dan bambo wa mwana wanga akalembe izi. Aaah 😭 adayamba kulira nthawi yomweyo. Ndipo amayi ake ataona adafunsa nati; mwana wanga ndichani? Koma iye adayankha uku akulira😭 nati; amayi, ndinalakwa chani ine? Dan watumiza kalata kuti wapeza mkazi wina ndipo sakundifunanso ayi. Heeeey! Chani? Ayi ayi ayi mwina wawerenga kuipa mwana wanga. Ndizoona amayi ndizomwe walemba apatu.

Nthawi yomweyo, amayi ake a Loney aja BP inachuta nagwa pansi pompo kumwalira chifukwa cha kalatayo. Lone adalira kwambiri limodzi ndi sister wake Tereza. Ndipo izi zidali zopweteka kwambiri kwa anawa onse komanso mitima yao idali yosweka ndithu💔. Anthu othandiza anabwera kuzathandiza ana aja kuika mwambo wa maliro a amayi awo. Zitatha zonse, Loney adamvanso zoti anti ake a Dan akubwerera kunja ndipo anaganiza zobweza kalata yomwe adalemba Dan kumyankha.

Ndipo Loney adalemba motere: wokondedwa mfumu yanga, mulibwanji? Ine kunu ndilibwino ndithu. Ndafuna ndithokoze chifukwa cha kalata yanu yomwe mudalemba. Ndidalandira ndipo zikomo kwambiri zonse mudalemba ndidawerenga koma choti mdziwe ndichakuti ndimakukondani kwambiri. Ndine Lonely, zikomo. Koma chifukwa choti padalibe munthu womtumiza kalatayo adanyamuka yekha Loney kupita ku palace kwa mfumu kuja kukasiya kalata ija. Atafika kuja adagogoda pa gate ndipo mulonda adatsegula nafunsa kuti ukufuna chani?

Koma Loney adayankha nati, ndifuna ndikumane ndi Queen ndili ndi uthenga wao. Atawaitana amfumukazi aja adaona kuti nfi Loney. Ndipo adangofikira kuti ukufuna chani kaumphawi iwe? Ndipo adati; ndabwera kudzasiya kalata yanga yopita kwa Prince kuyankhzo zomwe adalemba pa kalata yake. Kenako mayi mfumu adati; bweretsa kuno kalatayo ndipo zipita pompano. Loney adangosiya kalata yake ija nkubwerako. Atabwerako Loney uja, amfumukazi aja adalowa kuchipinda kwao natsegula kalata ija naiwerenga yonse. Kenako adaganizaso zosintha kalata ija isanafike kwa Prince mwana wao.

Adaitana mmodzi mwa atsikana ogwira ntchito ku palace kuja namuuza kuti akatenge cholembera ndi polemba pake. Atatenga mtsikana uja, amfumukazi adayamba kumuuza kuti yamba kulemba kalata chonchi: Wokondedwa mfumu yanga, kaya muli bwanji inetu kuno ndili bwino kwambiri. Kalata yanu ndidalandira zikomo. Koma ndifuna ndikuuzeni kuti pano ndaona kuti zabanja ndi inu sindikwanitsa ndiye ine ndidapeza mwamuna yemwe andikwatire pompano ndipo tikukhala kunja. Ndafuna ndikudziwitseni zomwezi. Koma mwana wanu alibwino ndithu ndiponso wakula pano. Zikomo kwambiri ine Loney💔.

Okondedwa awerengi zonse zinalembedwa apa adali maganizo a mfumukazi poti samafuna mwana wao akwatirane ndi banjali. Amayi omwe anatenga kalata aja adanyamuka ulendo wao wopita ku UK komanso ananyamula Kalata ija kuti akapatse Prince Dan poti samadziwa chilichonse kuti chibaluwa alemba ndi a queen. Amayi aja atafika ku UK kuja adamudziwitsa Dan kuti amunyamulira kalata yake kuchoka kwa Loney wachikondi wake. Apa Dan adasangalala kwambiri kuti amvako nkhani zachikondi. Kenako anapita kukatenga kalata ija kwa anti ake aja. Atatenga adabwerera kunyumba kwake nalowa kuchipinda kuyamba kuwerenga kalata ija. Atawerenga kalata ija anangogwira manja kumutu yekha yekha mnyumba mtima wake utaswekeratu kusala tiziduswa tingapo.

Kenako Dan mtima sadaugwire ndipo adaimbira foni mayi ake nawafotokodzera zonse zidali mkalata muja. Ndipo amayi adati; mwana wanga ndimamva chisoni kuti ndikuuze za Loney bwenzi lako. Loney uja adasintha pano ndipo ali ndi mwamuna moti ndikunenena pano kaya mawa ndamva kuti akuchoka mmudzi muno kupita kunja. Komaso mwana wanga mphekesera zikuti ati mwana uja alinayo siwako ayi. Amalankhula choncho a mfumukazi motsitsa mau kuti amfumu angawamve. Ndipo adapitiriza nati; osadandaula mwana wanga Prince ndakupezera mkazi wkumaloto kwako ndipo ndiwokongola komanso wakhalidwe moti ubwere uzapange ukwati kaye...hehehe my son I can't wait to see utatsoka ulusi😊😀 adatero mayi mfumu kunyengerera kuti mwana wao akwatire chisankho chao osati chake.

Koma Prince Dan adati; chabwino amayi ndakumvani koma Loney ndinamkonda kwambiri amayi. Osadandaula mwana wanga or Annabel yemwe ndakupedzera udzamkonda ndithu. Adatero mayi mfumu aja kuuza mwanawao. Koma iye adati; Ok chabwino amayi poti; Ndichikondi chokha chomwe chimapoletsa mabala achikondi...ndakumvani ndithu mwezi wamawa ndikubwera ndithu. Kenako Dan anadula foni ija kuyamba kulingalira zoti achite. Koma Loney kumudzi kuja adayamba business yogulitsa makala limodzi ndi sister wake Tereza komanso mwana wake Shamack chifukwa choti adalibe kopita kulikonse ayi.

Ndipo Annabel uja amapita ku palace kuja kukachezapo nawo mayi mfumu aja kenako amamulimbikitsa kuti Prince akubwera posachedwa azikhala okonzeka. Mwa ichi adali wosangalala kwambiri Annabel ngakhale kuti Prince Dan sadalankhulanepo naye kapena kuonanapo. Tsiku loti Prince Dan akubwera adamuuza Annabel nati; mawa Dan akubwera mwana wanga kudzapanga ukwati ndi iwe.

Kutacha mawa Annabel anayamba kumva ku anthu kuti Prince Dan wabwera. Ndipo pomwepo adanyamuka ndi mnzake kupita ku Palace kuja. Atafika kuja, atsikana ogwira ntchito ku palace adakaudza a mfumukazi kuti kwabwera Annabel ndipo adati akamuuze alowe mnyumba. Atalowa Annabel uja, amfumukazi aja adauza mnzake wa Annabel kuti akuyenera kumapita chifukwa Annabel akuyenera kucheza ndi mwamuna wake uja. Kenako naonso mfumukazi adakalowa kuchipinda kwao nasiya Annabel ndi Prince Dan awiri akucheza. Koma Prince Dan adati........

Next.........

Tiyeni tione part 3 kuti kuli zotani. Kodi Dan adati chani kwa Annabel? Tikhalire limodzi pompano..please DG don't forget to like and comment.

Zikomo🙏🙏

*TIDZAFERA LIMODZI IWE NDI INE* __PART 01__Umu mudali mwina momwe mudali mwana wamfumu yemwe ankatchedwa Prince Dan.  Ko...
19/10/2024

*TIDZAFERA LIMODZI IWE NDI INE*

__PART 01__

Umu mudali mwina momwe mudali mwana wamfumu yemwe ankatchedwa Prince Dan. Komanso mmudzi mwina mudali mtsikana wina yemwe ankatchedwa Lonely mwachidule ankamuti Loney. Prince Dan adali wochokera kubanja lachifumu pamene Loney adali wochokera kubanja losauka.

Anthu zidachitika kuti Prince Dan adamkonda kwambiri Loney ndipo anamfunsira kukhala mnzake(chibwenzi). Ndipo Loney adamulora Dani. Ubwebzi wa awiriwa umayenda bwino popanda chovuta chilichonse mpakana linafika tsiku lomwe Loney uja adadzindikira kuti ali ndi mimba. Atadziwa izi, adamuuza Prince Dan zoti ali ndi mimba yake. Ataudzidwa Dan adati; palibe vuto iwe ndi ine tidzafera limodzi sindingakusiye ayi ndipo ndikulonjeza. Ndi mau amenewa Lonenly adalimbikitsika mumtima mwake.

Koma Dan adaganiza zokawauza mayi ake. Ndipo atakawauza amayi ake aja, adali okwiya kwambiri nati: mwana wanga sungakwatire mmphawi ngati amene uja ayi. Komanso apa ndakusinthira sukulu ukamalizira sukulu yako kunja ku UK. Amayiwa amalankhula izi kufuna kungomuthawisiramo mwana wao kuti asakwatire Loney uja. Posakhalitsa Dan adapita kwa Loney kukamufotokozera kuti akupita kunja kukamaliza maphunziro ake.

Koma atamuuza, Loney adati; nanga ine ndi mimbayi ndipanga bwanji Dan chifukwa amayi anga ndawauza chilichonse ndipo avomera. Koma Dan adatu; usadandaule Loney ndinakulonjeza kale kuti tidzafera limodzi iwe ndi ine. Ndiye ndikafika kunja ndizikayesesa kulemba ndi kukutumizira ma kalata kuti mtima wako uzindikire kuti ndinakukonda. Anthuwa adasanzikana onse awiri ndipo Dan adanyamuka ulendo wake wopita ku UK kukamaliza maphunzira ake. Lonely adali mtsikana yemwe ankakhala ndi mayi wake komanso sister wake chifukwa bambo ake adamwalira iye ali mwana.

Nthawi iyi moyo unaliko bwino chifukwa ankalimbikitsika kuti adzakhala mfumukazi tsiku lina kutsogolo. Patapita zaka ziwiri, mwana wake wa Loney anali atabadwa ndi kukulako ndithu. Koma kwa Dan kudatsala zaka zitatu kuti amalize maphunziro ake. Ndipo tsiku lina, komwe kumakhala Dan kuja ku UK anti ake adali ndi ulendi wopita kumudzi kwao mmudzi momwe amachokera Dan muja. Ndipo Dan ataona adati; uwu ndi mwayi wapadera kuti nditumize kalata akapase wachikondi wanga Loney. Kenako Dan uja adakawauza anti ake aja kuti akamapita amtengereko kalata akapasire Loney ndipo anati; vuto palibe prince.

Kenako Dan adalemba kalata yachikondi nakawapatsa anti ake aja kuti akaptsire Loney. Anti ake adaitenga kalata ija naisunga. Tsiku labulendo wao litakwana, anti ake aja adanyamukankupita kumudzi kokaona anthu chifukwa adali atakhalitsa kudziko lakunja. Atafika kumudzi kuja, anti aja adakhala masiku awiri lachitatu adanyamuka kuti akampatsire kalata ija Lonely. Asadafike kwa Loney uja, adadzera kaye kwa mfumu kuti awaoneretu mwina apitanso posachedwa kubwerera kunja.

Atafika kwa mfumu kuja adawapeza ndithu anthu onse nawalandira nasangalala onse. Kenako adati; Mfumukazi ndayenera kupita sono poti ndizera kwa Loney kuja ndikampatsire kalata yake wanditumiza ndi Prince mwana wanu. Oooh ndizotero vuto palibe mwanawanga bweretsa ndikampatsa ine chifukwa ndikupitanso komweko ndifuna ndikamuone. Adatero mayi fumu aja kuuza mzukulu wao uja. Ndipo iye adati; zikomo kwambiri mayi wanga mwandipeputsa ndithu. Basi apa ndizipita tizaonanaso ndikabweranso. Adatero mzukulu wao uja. Kenako adanyamuka nkumapita kwao.

Amayi ake a Prince Dan aja adatsegula kalata ija naiwerenga yonse. Atamaliza kuwerenga kalata ija adaing'amba pakati nakaitaya amfumu osadziwa chilichonse. Kenako adapita kwa mlonda mmodzi yemwe ankamukhulupira kwambiri namuuza kuti akuyenera kutenga cholembera komanso pepala alembe zomwe atamuuzezo. Ndipo atatenga pepala ndi cholembera adamuuza kuti ulembe motere; wokondedwa Loney, mdaona kuti iwe ndi ine sitingakhalenso limodzi ndasintha maganizo anga. Sindikukwatiranso chifukwa ndidamva kuti mwanayo siwanga ayi. Ndiye ine sindingalere mwana wa wina. Ndiye ndipeza mkazi wina naweso peza mwamuna wina. Mwachidule ndingoti mkazi ndinampeza kale konkuno. Zikomo kwambiri ndine Dan.💔💔

Okondedwa mau onsewa analembedwa ndi mfumukazi chifukwa samafuna kuti mwana wao akwatire Lonely uja. Ndipo adatumiza mlonda uja kukapereka kalata ija kwa Loney. Atafika kuja adampeza Loney ndi amayi ake ali khale pakhonde. Kenako adaodira nalowa mkati. Ndipo adamlonjera bwino nati ndikwabwino ndatumidwa kuti ndizasiye chibaluwa ichi walemba olemekezeka Prince Dan anatumiza anti ake. Ndiye iwo atopa nkona mayi fumu andituma ine. Zikomo adatero napereka nkubwerako. Loney adali ndi chimwemwe kwambiri poganizira chikondi chao. Atatsegula nayamba kuwerenga adati..........

Next..........

Tiyeni tione part 2 kuti kunali zotani.

Zikomo awerengi nonse. Pempho ndiloti anthunu mumaikonda nkhani poyamba ndikupereka ma comment anu koma ma part akumapeto simpereka ma comments kapena ma like ndiye sizimalimbikitsa zotere awa ndi macheza macheza kuti akome pafunika tonse tizicheza popereka ndemanga zanu. Zimagwetsa ulesi kulemba ngati anthu sakukulimbikitsa. Ndiye chonde tiyeni ticheze limodzi.

Zikomo.

*TIDZAFERA LIMODZI IWE NDI INE* __PART 02__Okondedwa awerengi nonse, mongokumbutsana mu part 1 tinalekeza pomwe mayi mfu...
19/10/2024

*TIDZAFERA LIMODZI IWE NDI INE*

__PART 02__

Okondedwa awerengi nonse, mongokumbutsana mu part 1 tinalekeza pomwe mayi mfumu aja adasintha kalata wachikondi kukhala wachidani ndipo adatuma mlonda kuti akapasire Loney uja. Ndipo atalandira kalata uja Loney adali ndi chimwemwe poganizira chikondi chao. Koma atatsegula kuyamba kuwerenga adati;........

Tipitirizee......

Ndipo mlonda uja adachoka napita ku palace. Ndipo Loney adayamba kuwerenga kalata uja. Akuwerenga kalata chonchija adati; zitheka bwanji kuti Dan bambo wa mwana wanga akalembe izi. Aaah 😭 adayamba kulira nthawi yomweyo. Ndipo amayi ake ataona adafunsa nati; mwana wanga ndichani? Koma iye adayankha uku akulira😭 nati; amayi, ndinalakwa chani ine? Dan watumiza kalata kuti wapeza mkazi wina ndipo sakundifunanso ayi. Heeeey! Chani? Ayi ayi ayi mwina wawerenga kuipa mwana wanga. Ndizoona amayi ndizomwe walemba apatu.

Nthawi yomweyo, amayi ake a Loney aja BP inachuta nagwa pansi pompo kumwalira chifukwa cha kalatayo. Lone adalira kwambiri limodzi ndi sister wake Tereza. Ndipo izi zidali zopweteka kwambiri kwa anawa onse komanso mitima yao idali yosweka ndithu💔. Anthu othandiza anabwera kuzathandiza ana aja kuika mwambo wa maliro a amayi awo. Zitatha zonse, Loney adamvanso zoti anti ake a Dan akubwerera kunja ndipo anaganiza zobweza kalata yomwe adalemba Dan kumyankha.

Ndipo Loney adalemba motere: wokondedwa mfumu yanga, mulibwanji? Ine kunu ndilibwino ndithu. Ndafuna ndithokoze chifukwa cha kalata yanu yomwe mudalemba. Ndidalandira ndipo zikomo kwambiri zonse mudalemba ndidawerenga koma choti mdziwe ndichakuti ndimakukondani kwambiri. Ndine Lonely, zikomo. Koma chifukwa choti padalibe munthu womtumiza kalatayo adanyamuka yekha Loney kupita ku palace kwa mfumu kuja kukasiya kalata ija. Atafika kuja adagogoda pa gate ndipo mulonda adatsegula nafunsa kuti ukufuna chani?

Koma Loney adayankha nati, ndifuna ndikumane ndi Queen ndili ndi uthenga wao. Atawaitana amfumukazi aja adaona kuti nfi Loney. Ndipo adangofikira kuti ukufuna chani kaumphawi iwe? Ndipo adati; ndabwera kudzasiya kalata yanga yopita kwa Prince kuyankhzo zomwe adalemba pa kalata yake. Kenako mayi mfumu adati; bweretsa kuno kalatayo ndipo zipita pompano. Loney adangosiya kalata yake ija nkubwerako. Atabwerako Loney uja, amfumukazi aja adalowa kuchipinda kwao natsegula kalata ija naiwerenga yonse. Kenako adaganizaso zosintha kalata ija isanafike kwa Prince mwana wao.

Adaitana mmodzi mwa atsikana ogwira ntchito ku palace kuja namuuza kuti akatenge cholembera ndi polemba pake. Atatenga mtsikana uja, amfumukazi adayamba kumuuza kuti yamba kulemba kalata chonchi: Wokondedwa mfumu yanga, kaya muli bwanji inetu kuno ndili bwino kwambiri. Kalata yanu ndidalandira zikomo. Koma ndifuna ndikuuzeni kuti pano ndaona kuti zabanja ndi inu sindikwanitsa ndiye ine ndidapeza mwamuna yemwe andikwatire pompano ndipo tikukhala kunja. Ndafuna ndikudziwitseni zomwezi. Koma mwana wanu alibwino ndithu ndiponso wakula pano. Zikomo kwambiri ine Loney💔.

Okondedwa awerengi zonse zinalembedwa apa adali maganizo a mfumukazi poti samafuna mwana wao akwatirane ndi banjali. Amayi omwe anatenga kalata aja adanyamuka ulendo wao wopita ku UK komanso ananyamula Kalata ija kuti akapatse Prince Dan poti samadziwa chilichonse kuti chibaluwa alemba ndi a queen. Amayi aja atafika ku UK kuja adamudziwitsa Dan kuti amunyamulira kalata yake kuchoka kwa Loney wachikondi wake. Apa Dan adasangalala kwambiri kuti amvako nkhani zachikondi. Kenako anapita kukatenga kalata ija kwa anti ake aja. Atatenga adabwerera kunyumba kwake nalowa kuchipinda kuyamba kuwerenga kalata ija. Atawerenga kalata ija anangogwira manja kumutu yekha yekha mnyumba mtima wake utaswekeratu kusala tiziduswa tingapo.

Kenako Dan mtima sadaugwire ndipo adaimbira foni mayi ake nawafotokodzera zonse zidali mkalata muja. Ndipo amayi adati; mwana wanga ndimamva chisoni kuti ndikuuze za Loney bwenzi lako. Loney uja adasintha pano ndipo ali ndi mwamuna moti ndikunenena pano kaya mawa ndamva kuti akuchoka mmudzi muno kupita kunja. Komaso mwana wanga mphekesera zikuti ati mwana uja alinayo siwako ayi. Amalankhula choncho a mfumukazi motsitsa mau kuti amfumu angawamve. Ndipo adapitiriza nati; osadandaula mwana wanga Prince ndakupezera mkazi wkumaloto kwako ndipo ndiwokongola komanso wakhalidwe moti ubwere uzapange ukwati kaye...hehehe my son I can't wait to see utatsoka ulusi😊😀 adatero mayi mfumu kunyengerera kuti mwana wao akwatire chisankho chao osati chake.

Koma Prince Dan adati; chabwino amayi ndakumvani koma Loney ndinamkonda kwambiri amayi. Osadandaula mwana wanga or Annabel yemwe ndakupedzera udzamkonda ndithu. Adatero mayi mfumu aja kuuza mwanawao. Koma iye adati; Ok chabwino amayi poti; Ndichikondi chokha chomwe chimapoletsa mabala achikondi...ndakumvani ndithu mwezi wamawa ndikubwera ndithu. Kenako Dan anadula foni ija kuyamba kulingalira zoti achite. Koma Loney kumudzi kuja adayamba business yogulitsa makala limodzi ndi sister wake Tereza komanso mwana wake Shamack chifukwa choti adalibe kopita kulikonse ayi.

Ndipo Annabel uja amapita ku palace kuja kukachezapo nawo mayi mfumu aja kenako amamulimbikitsa kuti Prince akubwera posachedwa azikhala okonzeka. Mwa ichi adali wosangalala kwambiri Annabel ngakhale kuti Prince Dan sadalankhulanepo naye kapena kuonanapo. Tsiku loti Prince Dan akubwera adamuuza Annabel nati; mawa Dan akubwera mwana wanga kudzapanga ukwati ndi iwe.

Kutacha mawa Annabel anayamba kumva ku anthu kuti Prince Dan wabwera. Ndipo pomwepo adanyamuka ndi mnzake kupita ku Palace kuja. Atafika kuja, atsikana ogwira ntchito ku palace adakaudza a mfumukazi kuti kwabwera Annabel ndipo adati akamuuze alowe mnyumba. Atalowa Annabel uja, amfumukazi aja adauza mnzake wa Annabel kuti akuyenera kumapita chifukwa Annabel akuyenera kucheza ndi mwamuna wake uja. Kenako naonso mfumukazi adakalowa kuchipinda kwao nasiya Annabel ndi Prince Dan awiri akucheza. Koma Prince Dan adati........

Next.........

Tiyeni tione part 3 kuti kuli zotani. Kodi Dan adati chani kwa Annabel? Tikhalire limodzi pompano..please don't forget to like and comment.

Zikomo🙏🙏

Address

Nkhani Zophunzitsa, Kudziwitsa Komanso Kusangalatsa
Pretoria

Website

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when Kufuna Kutchuka and Other Stories posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Shortcuts

Share

Category